14
Ku Ikoniya
1 Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira.
2 Koma Ayuda amene anakana kukhulupirira anawutsa anthu a mitundu ina nawononga maganizo awo kutsutsana ndi abale.
3 Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo.
4 Anthu a mu mzindamo anagawikana; ena anali mbali ya Ayuda, ena mbali ya atumwi.
5 Pamenepo anthu a mitundu ina ndi Ayuda, pamodzi ndi atsogoleri awo anakonza chiwembu choti azunze atumwiwo ndi kuwagenda ndi miyala.
6 Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo,
7 kumene anapitiriza kulalikira Uthenga Wabwino.
Ku Lusitra ndi ku Derbe
8 Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake.
9 Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho.
10 Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda.
11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!”
12 Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula.
13 Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.
14 Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti,
15 “Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
16 Kale Iye analola anthu a mitundu ina yonse kutsata njira zawozawo.
17 Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.”
18 Ngakhale ndi mawu awa, anavutika kuletsa gulu la anthu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19 Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa.
20 Koma ophunzira atamuzungulira, Pauloyo anayimirira nalowanso mu mzindawo. Mmawa mwake iye ndi Barnaba anachoka ndi kupita ku Derbe.
Paulo ndi Barnaba Abwerera ku Antiokeya wa ku Siriya
21 Iwo analalikira Uthenga Wabwino mu mzindawo ndipo anthu ambiri anatembenuka mtima ndi kukhala ophunzira. Kenaka anabwerera ku Lusitra, ku Ikoniya ndi ku Antiokeya.
22 Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”
23 Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira.
24 Atadutsa Pisidiya, anafika ku Pamfiliya.
25 Atalalikira Mawu ku Perga, anapita ku Ataliya.
26 Ku Ataliyako, anakwera sitima ya pamadzi kubwerera ku Antiokeya kumene anayitanidwa mwachisomo cha Mulungu kuti agwire ntchito imene tsopano anali atayitsiriza.
27 Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro.
28 Ndipo anakhala kumeneko ndi ophunzira nthawi yayitali.