23
1 Paulo anayangʼanitsitsa anthu a Bwalo Lalikulu nati, “Abale anga, ndakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu mpaka lero lino.”
2 Chifukwa cha mawu amenewa, mkulu wa ansembe Ananiya analamulira amene anali pafupi ndi Paulo kuti amumenye pakamwa.
3 Pamenepo Paulo anamuwuza kuti, “Mulungu adzakukantha, iwe munthu wachiphamaso! Wakhala pamenepo kuti undiweruze ine monga mwalamulo, koma iweyo ukuphwanya lamulolo polamulira kuti andimenye!”
4 Anthu amene anayimirira pafupi ndi Paulo anati, “Bwanji ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?”
5 Paulo anayankha nati, “Abale, ine sindinazindikire kuti ndi mkulu wa ansembe; pakuti kunalembedwa kuti, ‘Usayankhule zoyipa kwa mtsogoleri wa anthu ako.’ ”
6 Paulo atazindikira kuti ena mwa iwo anali Asaduki ndiponso ena anali Afarisi, anafuwula mʼbwalo muja kuti, “Abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.”
7 Iye atanena zimenezi, mkangano unabuka pakati pa Afarisi ndi Asaduki mpaka anthu kugawikana.
8 Asaduki amati kulibe kuuka kwa akufa, kulibenso ngakhale angelo kapena mizimu, koma Afarisi amakhulupirira zonsezi.
9 Panali phokoso lalikulu, ndipo aphunzitsi ena amalamulo amene anali a gulu la Afarisi anayimirira natsutsa kwambiri. Iwo anati, “Ife sitikupeza cholakwa ndi munthu uyu, chifukwa mwina ndi mzimu kapena mngelo amene wayankhula naye.”
10 Mkangano unakula kwambiri kotero kuti mkulu wa asilikali anachita mantha kuti mwina anthu angakhadzule Paulo. Iye analamulira asilikali ake apite kukamuchotsa pakati pawo mwamphamvu ndi kubwera naye ku malo a asilikaliwo.
11 Usiku omwewo Ambuye anayimirira pambali pa Paulo nati, “Limba mtima! Monga wandichitira Ine umboni mu Yerusalemu, moteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.”
Ayuda Achita Chiwembu Paulo
12 Kutacha Ayuda ena anakonza chiwembu ndipo analumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo.
13 Anthu amene anakonza chiwembuchi analipo makumi anayi.
14 Iwo anapita kwa akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda nakawawuza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitidya kalikonse mpaka titapha Paulo.
15 Tsopano inu pamodzi ndi akuluakulu a Bwalo Lalikulu mupemphe mkulu wa asilikali kuti akubweretsereni Paulo ngati kuti mukufuna kudziwa bwino za mlandu wake. Ife takonzeka kudzamupha asanafike kumeneko.”
16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, anapita ku malo a asilikali aja namufotokozera Paulo.
17 Paulo anayitana mmodzi wa wolamulira asilikali 100 aja, namuwuza kuti, “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali. Iyeyu ali ndi mawu oti akamuwuze.”
18 Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”
19 Mkulu wa asilikali uja anagwira dzanja mnyamatayo napita naye paseli ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti undiwuze chiyani?”
20 Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye.
21 Inu musawamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anayi amene akumudikirira pa njira. Iwo alumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Panopa ndi okonzeka kale, akungodikira kuti muwavomere pempho lawo.”
22 Mkulu wa asilikaliyo anawuza mnyamatayo kuti apite koma anamuchenjeza kuti, “Usawuze munthu aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
Paulo Apita ku Kaisareya
23 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anayitana awiri a asilikali olamulira asilikali 100 nawalamula kuti, “Uzani asilikali 200, asilikali 70 okwera pa akavalo ndi 200 onyamula mikondo kuti akonzeke kupita ku Kaisareya usiku omwe uno nthawi ya 9 koloko.
24 Mumukonzerenso Paulo akavalo woti akwerepo kuti akafike bwino kwa bwanamkubwa Felike.”
25 Iye analemba kalata iyi:
26 Ine Klaudiyo Lusiya,
Kwa wolemekezeka, bwanamkubwa Felike:
Ndikupereka moni.
27 Munthuyo Ayuda anamugwira ndipo anali pafupi kumupha, koma ine ndinapita ndi asilikali nʼkukamulanditsa pakuti ndinamva kuti ndi nzika ya Chiroma.
28 Ndinkafuna kudziwa mlandu umene anapalamula, choncho ndinapita naye ku Bwalo lawo Lalikulu.
29 Ine ndinapeza kuti amamuyimba mlandu wa nkhani ya malamulo awo, koma panalibe mlandu woyenera kumuphera kapena kumuyika mʼndende.
30 Nditawuzidwa kuti amukonzera chiwembu munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga. Ine ndalamulanso amene akumuyimba mlanduwo kuti abwere kwa inu kudzafotokoza nkhaniyo.
31 Pamenepo asilikali aja anatenga Paulo monga anawalamulira napita naye ku Antipatri usiku.
32 Mmawa mwake iwo anabwerera ku malo a asilikali nasiya okwera pa akavalo kuti apitirire ndi Paulo.
33 Asilikali okwera pa akavalowo atafika ku Kaisareya anapereka kalatayo kwa bwanamkubwa, namuperekanso Paulo.
34 Bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anamufunsa Paulo za dera limene amachokera. Atazindikira kuti amachokera ku Kilikiya,
35 iye anati, “Ndidzamva mlandu wako okuyimba mlandu akabwera kuno.” Ndipo analamulira kuti asilikali adzimulondera Paulo ku nyumba ya mfumu Herode.