4
Petro ndi Yohane ku Bwalo la Akulu
Pamene Petro ndi Yohane amayankhula ndi anthu, kunabwera ansembe, mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndiponso Asaduki. Iwo anakhumudwa kwambiri chifukwa atumwiwo amaphunzitsa anthu ndi kumalalikira za kuuka kwa akufa mwa Yesu. Iwo anagwira Petro ndi Yohane, popeza kunali kutada, anawayika mʼndende mpaka mmawa mwake. Koma anthu ambiri amene anamva uthenga anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha anthu chinakwana 5,000.
Mmawa mwake olamulira, akulu ndi aphunzitsi a malamulo anasonkhana mu Yerusalemu. Panali Anasi, Mkulu wa ansembe, Kayafa, Yohane ndi Alekisandro ndi ana a banja la mkulu wa ansembe. Iwo anayimiritsa Petro ndi Yohane patsogolo pawo nayamba kuwafunsa kuti, “Kodi munachita zimenezi ndi mphamvu yanji kapena mʼdzina la yani?”
Petro wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anawawuza kuti, “Inu olamulira ndi akulu! Ngati ife tikufunsidwa lero chifukwa cha ntchito yabwino imene yachitika pa munthu wolumala miyendo ndi mmene iye anachiritsidwira, 10 tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. 11 Iye ndi
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana,
umenewo wasanduka mwala wa pa ngodya!’
12 Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”
13 Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu. 14 Koma popeza iwo amamuona munthu amene anachiritsidwa atayima pamodzi ndi iwo, palibe chimene akananena. 15 Chifukwa chake anawalamula kuti atuluke mʼbwalo la milandu ndipo akulu abwalowo anayamba kukambirana. 16 Iwo anafunsana kuti, “Kodi anthuwa tichite nawo chiyani? Pakuti aliyense okhala mu Yerusalemu akudziwa kuti achita chodabwitsachi, ndipo ife sitingathe kukana. 17 Koma kuti mbiriyi isapitirire kuwanda pakati pa anthu, ife tiwachenjeze anthu amenewa kuti asayankhulenso kwa wina aliyense mʼdzina la Yesu.”
18 Pamenepo anawayitananso ndipo anawalamula kuti asayankhule kapena kuphunzitsa konse mʼdzina la Yesu. 19 Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. 20 Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”
21 Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika. 22 Ndipo munthu amene anachiritsidwayo anali ndi zaka makumi anayi.
Okhulupirira Apemphera
23 Atamasulidwa Petro ndi Yohane anapita kwa anzawo ndipo anawafotokozera zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu anawawuza. 24 Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo. 25 Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti,
“ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu,
ndipo akonzekera kuchita zopandapake?
26 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
ndi wodzozedwa wakeyo.’
27 Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza. 28 Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike. 29 Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima. 30 Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.”
31 Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.
Okhulupirira Agawana Zinthu Zawo
32 Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho. 33 Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka. 34 Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo 35 ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.
36 Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso, 37 anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.