16
Ndalama Zothandizira Akhristu a ku Yerusalemu
1 Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite.
2 Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha.
3 Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu.
4 Ngati kutaoneka kuti nʼkoyenera kuti ndipite nawo, adzapita nane limodzi.
Paulo Afotokoza za Maulendo ake ndi Zina
5 Ndidzafika kwanuko nditadutsa ku Makedoniya pakuti ndikuyembekezera kudzera ku Makedoniyako.
6 Mwina ndidzakhala nanu kanthawi kochepa kapenanso nyengo yonse yozizira, kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite.
7 Sindikufuna kuti ndikuoneni tsopano mongodutsa chabe, koma ndikuyembekezera kudzakhala nanu kwa kanthawi, ngati Ambuye alola.
8 Koma ndikhala ndili ku Efeso mpaka nthawi ya Pentekosite,
9 pakuti mwayi waukulu wapezeka woti nʼkugwira ntchito yaphindu, koma pali ambiri amene akutsutsana nane.
10 Ngati Timoteyo afike kwanuko, onetsetsani kuti pasakhale zina zomuchititsa mantha pamene ali pakati panu, pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye monga ine.
11 Wina aliyense asamunyoze. Muthandizeni kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwereranso kuli ine. Ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.
12 Tsono kunena za mʼbale wathu, Apolo, ndinamuwumiriza kwambiri kuti abwere kwa inu abale, ndipo iye sanafune kupita tsopano. Koma akadzapeza mpata wabwino adzabwera.
13 Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.
14 Chitani zonse mwachikondi.
15 Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale,
16 kuti muziwamvera anthu oterewa, ndiponso aliyense wogwira nawo ntchitoyi modzipereka.
17 Ndikondwera kuti Stefano, Fortunato ndi Akayiko afika, chifukwa akhala akundithandiza pakuti inu simuli nane.
18 Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu womwe. Anthu a mtundu oterewa ngofunika kuwalemekeza.
Mawu Otsiriza
19 Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni.
20 Abale onse kuno akupereka moni wawo. Patsanani moni wachikondi chenicheni.
21 Ineyo Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa mawu awa akuti moni.
22 Ngati wina sakonda Ambuye akhale wotembereredwa. Maranatha! (Ambuye athu bwerani)!
23 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi inu.
24 Chikondi changa chikhale ndi nonsenu mwa Khristu Yesu.