2
1 Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu.
2 Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo.
3 Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri.
4 Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu,
5 kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.
Nzeru Yochokera kwa Mzimu
6 Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha.
7 Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi.
8 Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero.
9 Komabe monga zalembedwa kuti,
“Palibe diso linaona,
palibe khutu linamva,
palibe amene anaganizira,
zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”
10 koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake.
Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe.
11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo.
12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere.
13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu.
14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu.
15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense.
16 Pakuti
“Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye,
kuti akhoza kumulangiza Iye.”
Koma tili nawo mtima wa Khristu.