6
1 Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe.
2 Pakuti akunena kuti,
“Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera,
ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza.
Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”
Masautso a Paulo
3 Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke.
4 Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa.
5 Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya;
6 pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi
7 ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo.
8 Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza.
9 Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa.
10 Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.
11 Tayankhula momasuka kwa inu, Akorinto, ndipo tanena zonse za kumtima kwathu.
12 Ife sitikukubisirani chikondi chathu pa inu, koma inu mukubisa chikondi chanu pa ife.
13 Pofuna kufanana zochita ndi kuyankhula monga kwa ana anga, nanunso muzinena za kukhosi kwanu.
Kukhala Pamodzi ndi Osakhulupirira
14 Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima?
15 Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira?
16 Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti,
“Ndidzakhala mwa iwo
ndipo ndidzayendayenda pakati pawo,
ndipo ndidzakhala Mulungu wawo,
ndipo adzakhala anthu anga.”
17 Nʼchifukwa chake
“Tulukani pakati pawo
ndi kudzipatula,
akutero Ambuye.
Musakhudze chodetsedwa chilichonse,
ndipo ndidzakulandirani.”
18 Ndipo
“Ndidzakhala Atate anu,
ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,
akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”