Danieli
1
Maphunziro a Danieli ku Babuloni
1 Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inabwera ndi kuzinga mzinda wa Yerusalemu ndi kuwuthira nkhondo.
2 Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake.
3 Tsono mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zake kuti abwere nawo ena mwa Aisraeli ochokera mʼbanja laufumu ndi la olemekezeka,
4 achinyamata wopanda chilema, okongola, aluso mu nzeru zonse, okhala ndi chidziwitso, achangu pophunzira, odziwa kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Ndipo anati awaphunzitsenso kuwerenga chiyankhulo cha Ababuloni.
5 Ndipo mfumu imawapatsa tsiku ndi tsiku gawo la chakudya ndi vinyo wa ku nyumba yaufumu, ndi kuti awaphunzitse kwa zaka zitatu, ndipo kenaka adzayambe kutumikira mfumu.
6 Pakati pa amenewa panali ena ochokera ku Yuda: Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya.
7 Mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina atsopano: Danieli anamutcha Belitesezara; Hananiya anamutcha Sadirake; Misaeli anamutcha Mesaki; ndi Azariya anamutcha Abedenego.
8 Koma Danieli anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya ndi vinyo wa mfumu, ndipo anapempha chilolezo kwa mkulu wa nduna za mfumu kuti asadzidetse mwa njira imeneyi.
9 Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli,
10 koma ndunayo inamuwuza Danieli kuti, “Ine ndikuchita mantha ndi mbuye wanga mfumu, amene wapereka chakudya ndi chakumwa chanu. Kodi akuoneni inu owonda kuposa anzanu a misinkhu yanu pa chifukwa chanji? Mfumu ikhoza kundidula mutu chifukwa cha iwe.”
11 Ndipo Danieli anati kwa kapitawo amene anali mkulu wa nduna za mfumu amene anamuyika kuti ayangʼanire Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya,
12 “Chonde mutiyese ife akapolo anu pa masiku khumi: mutipatse masamba okha kuti tidye ndi madzi akumwa.
13 Ndipo mudzafananize maonekedwe athu ndi a anyamata amene akudya chakudya cha mfumu, ndi kuti mudzachite ndi anyamata anu monga momwe mudzawaonere.”
14 Choncho anawavomera ndipo anawayesa pa masiku khumi.
15 Pakutha pa masiku khumi iwo anaoneka athanzi ndi odya bwino kuposa aliyense wa anyamata amene ankadya chakudya cha mfumu aja.
16 Choncho kapitawo anawachotsera chakudya ndi vinyo za ku nyumba yaufumu zija nawapatsa ndiwo zamasamba basi.
17 Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.
18 Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara.
19 Mfumu inayankhula nawo, ndipo panalibe wofanana ndi Danieli; Hananiya Misaeli ndi Azariya; Choncho analowa ndi kukhala otumikira mfumu.
20 Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso.
21 Ndipo Danieli anali kumeneko mpaka chaka choyamba cha ufumu wa Koresi.