10
Masomphenya a Danieli a Munthu
1 Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.
2 Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu.
3 Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.
4 Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, nditayima mʼmbali mwa mtsinje waukulu wa Tigirisi,
5 ndinakweza maso ndipo ndinaona kuti pafupi ndi ine panali munthu wochokera ku Ufazi atavala zovala zosalala ndi lamba wa golide woyengeka bwino mʼchiwuno mwake.
6 Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu.
7 Ine Danieli ndinali ndekha pamene ndinaona masomphenyawa; anthu amene anali ndi ine sanawaone, koma anadzazidwa ndi mantha kotero kuti anathawa ndi kukabisala.
8 Choncho ndinatsala ndekha, ndikuonetsetsa masomphenya a ulemererowa. Ndiye nkhope yanga inasinthika, ndinalefuka, ndipo ndinalibenso mphamvu.
9 Kenaka ndinamva iye akuyankhula, ndipo pamene ndinkamvetsera, ndinagwa chafufumimba ndi kugona tulo tofa nato.
10 Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi.
11 Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera.
12 Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo.
13 Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya.
14 Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”
15 Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena.
16 Kenaka wina wa maonekedwe ngati munthu anakhudza milomo yanga, ndipo ndinatsekula pakamwa panga ndi kuyamba kuyankhula. Ndinati kwa amene anayima patsogolo panga, “Ine ndasweka mtima chifukwa cha masomphenyawa mbuye wanga, ndipo ndalefuka.
17 Kodi ine mtumiki wamba wa mbuye wanga ndingathe bwanji kuyankhula ndi inu mbuye wanga? Mphamvu zanga zatha, ndipo ndikulephera kupuma.”
18 Kenaka wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso ndipo anandipatsa mphamvu.
19 Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.”
Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.”
20 Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera.
21 Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”