10
Miyala Ngati Yoyamba Ija
Pa nthawi imeneyo Yehova anati kwa ine, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo ubwere nayo kwa Ine ku phiri. Upangenso bokosi lamatabwa. Ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ndipo iwe ukuyenera kuyika miyalayo mʼbokosimo.”
Choncho ndinapanga bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo ndinapita ku phiri nditanyamula miyala iwiri mʼmanja mwanga. Yehova analemba pa miyala iwiriyo zimene analemba poyamba, Malamulo Khumi amene analengeza kwa inu pa phiri paja, mʼmoto, pa tsiku la msonkhano. Ndipo Yehova anawapereka kwa ine. Tsono ndinatsika ku phiri kuja ndi kuyika miyalayo mʼbokosi ndinapanga lija monga Yehova anandilamulira, ndipo panopa ili mʼmenemo.
Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake. Kuchokera kumeneko Aisraeli anapita ku Gudigoda, napitirira mpaka ku Yotibata, ku dziko la mitsinje ya madzi. Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero. Nʼchifukwa chake Alevi alibe gawo kapena cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo monga momwe Yehova Mulungu wanu anawawuzira.
10 Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni. 11 Yehova anati kwa ine, “Pita ndi kutsogolera anthuwa pa njira yawo, kuti alowe ndi kulandira dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndiwapatse.”
Kuopa Yehova
12 Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, 13 ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.
14 Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 15 Yehova anayika mtima wake pa makolo anu okha ndipo anawakondadi nasankha adzukulu awo mwa mitundu yonse pa dziko lapansi, kunena inuyo monga mulili lero. 16 Motero chitani mdulidwe wa mitima yanu ndipo musakhalenso opulupudza. 17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. 18 Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. 19 Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto. 20 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye. Mumukakamire Iyeyo ndi kuchita malumbiro anu mʼdzina lake. 21 Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija. 22 Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.