16
Paska
1 Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto.
2 Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake.
3 Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto.
4 Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.
5 Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani,
6 koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto.
7 Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu.
8 Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Chikondwerero cha Masabata
9 Muziwerenga masabata asanu ndi awiri kuyambira pamene mwatenga chikwakwa ndi kuyamba kumweta tirigu wachilili.
10 Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani
11 Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake.
12 Kumbukirani kuti inunso munali akapolo ku Igupto, ndiye muzitsatira malangizo awa mosamalitsa.
Chikondwerero cha Misasa
13 Mukatha kukolola tirigu wanu ndi kupsinya vinyo wanu, muzikhala ndi Chikondwerero cha Misasa kwa masiku asanu ndi awiri.
14 Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu.
15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
16 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake.
17 Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.
Oweruza
18 Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo.
19 Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.
20 Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Kupembedza Milungu Ina
21 Musazike mtengo wina uliwonse wa mafano a Asera pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu,
22 ndipo musayimike mwala wachipembedzo pakuti Yehova Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.