22
1 Ngati uwona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wako ikusochera, usayilekerere koma uyesetse kuyibwezera kwa iye.
2 Ngati mʼbale wakoyo sakhala pafupi kapena sukudziwa kuti ndi yandani, uyitengere ku nyumba kwako ndi kuyisamala mpaka mwini wake atayilondola ndipo umubwezere.
3 Uzitero ndithu ngati upeza bulu kapena mkanjo kapena chilichonse chimene chatayika. Osachilekerera.
4 Ngati wapeza bulu kapena ngʼombe ya mʼbale wako itagwa panjira, usayilekerere. Ithandize kuti idzuke.
5 Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi.
6 Ukapeza chisa cha mbalame mʼmphepete mwa msewu, kaya ndi mu mtengo kapena pansi, mbalame yayikazi itafungatira ana kapena mazira, usatenge mbalameyo pamodzi ndi ana ake omwe.
7 Anawo mukhoza kutenga koma onetsetsani kuti mayi wawo mwamutaya kuti apite, kuti zinthu zizikuyenderani bwino ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali.
8 Mukamanga nyumba yatsopano, mutchingire khonde lake la pa denga kuti inu musapezeke ndi mlandu wopha munthu ngati wina agwa kuchokera pa khonde la pa dengalo.
9 Musadzale mbewu zamitundu iwiri mʼmunda wanu wa mpesa, ngati mutero, si mbewu zanu zokha zimene zidzakhale zodetsedwa, komanso zipatso za mʼmunda wamphesawo.
10 Musatipule pogwiritsa ntchito ngʼombe ndi bulu pa goli limodzi.
11 Musamavale chovala chopangidwa mophatikiza ubweya ndi thonje.
12 Muzipanga mphonje mʼngodya za mkanjo umene mumavala.
Malamulo a Ukwati
13 Ngati munthu akwatira mkazi, ndipo atagona naye nʼkusamufunanso
14 namunyoza ndi kumuyipitsira dzina nʼkumati, “Ine ndinakwatira mkazi uyu, koma pamene ndinakhala naye, sindinachione chizindikiro cha unamwali wake,”
15 zikatero abambo ndi amayi ake ayenera kubweretsa chitsimikizo chakuti anali namwali kwa akuluakulu a mzinda ku chipata.
16 Abambo ake a mtsikanayo adzanene kwa akuluakuluwo kuti, “Ine ndinamupatsa munthu uyu mwana wanga wamkazi kuti amukwatire, koma sakumufunanso.
17 Tsopano wamunyoza ndipo wanena kuti, ‘Ine sindinapeze kuti mwana wanu wamkaziyu ndi namwali.’ Koma tsopano onani chitsimikizo ichi cha unamwali wa mwana wanga wamkazi.” Kenaka makolo a mtsikanayo adzaonetse kansalu kwa akuluakulu aja,
18 ndipo akuluakuluwo adzamugwire munthuyo namupatsa chilango.
19 Iwo adzamulipitse ndalama zasiliva zokwana 100 nazipereka kwa abambo a mtsikana, chifukwa munthu uyu wayipitsa dzina la mtsikana wa Chiisraeli. Ayenera kukhalabe mkazi wake ndipo asadzamuleke moyo wake wonse.
20 Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo kuti chitsimikizo cha unamwali wa mtsikanayo sichinapezeke,
21 iyeyu ayenera kumutengera pa khomo pa abambo ake pamene anthu a mu mzinda wake akamuphere ndi miyala. Iyeyo wachita chinthu chochititsa manyazi mu Israeli pochita chiwerewere akanali pa khomo pa abambo ake. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu.
22 Ngati munthu apezeka akugona ndi mkazi wa mwini wake, ayenera kuphedwa munthuyo pamodzi ndi mkazi yemwe wagona nayeyo. Muyenera kuchotsa zoyipa mu Israeli.
23 Ngati munthu mu mzinda akumana ndi mkazi yemwe anachita kale chinkhoswe nagona naye,
24 muwatengere awiriwo ku chipata cha mzinda ndi kuwapha ndi miyala. Aphedwe chifukwa mtsikanayo anali pafupi ndi anthu ndipo sanakuwe kuti ena amuthandize ndipo mwamunayo chifukwa anayipitsa mkazi wa mwini. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
25 Koma ngati munthu akumana ndi mkazi kutchire yemwe anachita kale chinkhoswe namugwiririra, mwamuna yekhayo ndiye woyenera kuphedwa.
26 Mtsikanayo musamuchite chilichonse, palibe tchimo limene wachita loti ayenera kuphedwa. Mlandu uwu ufanana ndi wa munthu amene alimbana ndi kupha mnzake woyandikana naye,
27 pakuti mwamunayo anamupeza mtsikanayo kutchire, ndipo ngakhale mtsikana wachinkhosweyo anakuwa, panalibe anamulanditsa.
28 Ngati munthu apezana ndi namwali woti sanachite chinkhoswe, namugwiririra, munthuyo nʼkupezeka,
29 ayenera kuwalipira abambo ake a namwaliyo ndalama za siliva makumi asanu. Iye ayenera kumukwatira mkaziyo chifukwa wamuyipitsa, ndipo sadzamulekanso moyo wake wonse.
30 Munthu asakwatire mkazi wa abambo ake pakuti ayenera kuchitira ulemu pogona pa abambo ake.