9
Pemphero la Ezara pa za Kukwatirana ndi a Mitundu Ina
1 Zitachitika izi, atsogoleri anabwera kwa ine nati, “Aisraeli, kuphatikizanso ansembe ndi Alevi, sanadzipatule ku makhalidwe onyansa a anthu a mitundu ina amene ayandikana nafe: Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aigupto ndi Aamori.
2 Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.”
3 Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa.
4 Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.
5 Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga
6 ndipo ndinapemphera kuti,
“Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo.
7 Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu.
8 “Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu.
9 Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu.
10 “Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, kodi tinganene chiyani titachita zoyipa zonsezi? Ife taphwanya malamulo anu
11 amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa.
12 Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’
13 “Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke,
14 kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka?
15 Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”