KALATA YACHIWIRI YA PAULO YOLEMBERA
ATESALONIKA
1
1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo.
Kulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
2 Chisomo ndi mtendere kwa inu kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.
Kuyamika ndi Pemphero
3 Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe.
4 Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo.
5 Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira.
6 Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo
7 ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.
8 Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.
9 Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake
10 pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu.
11 Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro.
12 Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.