3
Yesu ndi Wamkulu Kuposa Mose
1 Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.
2 Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.
3 Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo.
4 Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.
5 Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo.
6 Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.
Chenjezo pa Kusakhulupirira
7 Tsono monga Mzimu Woyera akuti,
“Lero mukamva mawu ake,
8 musawumitse mitima yanu
ngati munachitira pamene munawukira,
pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.
9 Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa,
ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita.
10 Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo,
ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,
ndipo iwo sadziwa njira zanga.’
11 Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti,
‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ”
12 Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
13 Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.
14 Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi.
15 Monga kunanenedwa kuti,
“Lero ngati mumva mawu ake,
musawumitse mitima yanu
ngati momwe munachitira pamene munawukira.”
16 Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto?
17 Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja?
18 Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja.
19 Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.