14
1 Yehova adzachitira chifundo Yakobo;
adzasankhanso Israeli
ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo.
Alendo adzabwera kudzakhala nawo
ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
2 Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli
ku dziko lawo.
Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja
kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.
Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.
Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
3 Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani,
4 mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,
Wopsinja uja watha!
Ukali wake uja watha!
5 Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,
Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
6 Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali
powamenya kosalekeza,
Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali
ndikuwazunza kosalekeza.
7 Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;
ndipo akuyimba mokondwa.
8 Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni
ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,
“Chigwetsedwere chako pansi,
palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
9 Ku manda kwatekeseka
kuti akulandire ukamabwera;
mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri
a dziko lapansi, yadzutsidwa.
Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu
ayimiritsidwa pa mipando yawo.
10 Onse adzayankha;
adzanena kwa iwe kuti,
“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;
Iwe wafanana ndi ife.”
11 Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,
pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;
mphutsi zayalana pogona pako
ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.
12 Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,
iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!
Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,
Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
13 Mu mtima mwako unkanena kuti,
“Ndidzakwera mpaka kumwamba;
ndidzakhazika mpando wanga waufumu
pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;
ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,
pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;
ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
15 Koma watsitsidwa mʼmanda
pansi penipeni pa dzenje.
16 Anthu akufa adzakupenyetsetsa
nadzamalingalira za iwe nʼkumati,
“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi
ndi kunjenjemeretsa maufumu,
17 munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu,
amene anagwetsa mizinda yake
ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”
18 Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu
aliyense mʼmanda akeake.
19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,
ngati nthambi yowola ndi yonyansa.
Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;
amene anabayidwa ndi lupanga,
anatsikira mʼdzenje lamiyala
ngati mtembo woponderezedwa.
20 Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu,
chifukwa unawononga dziko lako
ndi kupha anthu ako.
Zidzukulu za anthu oyipa
sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
21 Konzani malo woti muphere ana ake aamuna
chifukwa cha machimo a makolo awo;
kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi
ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
22 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.
Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.
Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”
akutero Yehova.
23 “Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu
ndiponso dambo lamatope;
ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Za Kulangidwa kwa Asiriya
24 Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti,
“Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho,
ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
25 Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;
ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;
ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,
ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
26 Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,
ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
27 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?
Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
Za Kulangidwa kwa Afilisti
28 Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:
29 Musakondwere inu Afilisti nonse
kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;
chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,
ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
30 Osaukitsitsa adzapeza chakudya
ndipo amphawi adzakhala mwamtendere.
Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,
ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
31 Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!
Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!
Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,
ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
32 Kodi tidzawayankha chiyani
amithenga a ku Filisitiya?
“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,
ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”