26
Nyimbo ya Matamando
Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.
Tili ndi mzinda wolimba.
Mulungu amawuteteza ndi zipupa
ndi malinga.
Tsekulani zipata za mzinda
kuti mtundu wolungama
ndi wokhulupirika ulowemo.
Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
Mudalireni Yehova mpaka muyaya,
chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.
Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,
iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,
amagumula makoma ake
ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
Mapazi a anthu akuwupondereza,
mapazi a anthu oponderezedwa,
mapazi anthu osauka.
 
Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,
Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.
Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,
ife timayembekezera Inu;
mitima yathu imakhumba kukumbukira
ndi kulemekeza dzina lanu.
Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;
nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.
Pamene muweruza dziko lapansi
anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
10 Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,
saphunzira chilungamo.
Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,
ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
11 Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,
koma iwo sakuliona dzanjalo.
Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;
ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
 
12 Yehova, mumatipatsa mtendere;
ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.
13 Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,
koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.
14 Iwo tsopano sadzadzukanso;
mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa
pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;
palibenso amene amawakumbukira.
15 Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;
mwauchulukitsa ndithu
ndipo mwalandirapo ulemu;
mwaukuza mbali zonse za dziko.
 
16 Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso;
pamene munawalanga,
iwo anapemphera kwa Inu.
17 Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira
amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu,
ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.
18 Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana,
koma sitinapindulepo kanthu,
kapena kupulumutsa dziko lapansi;
sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
 
19 Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo;
matupi awo adzadzuka.
Iwo amene ali ku fumbi tsopano
adzadzuka ndi kuyimba mosangalala.
Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera,
momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
 
20 Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanu
ndipo mukadzitsekere;
mukabisale kwa kanthawi kochepa
mpaka ukali wake utatha.
21 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala;
akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo.
Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo;
dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.