37
Hezekiya Apempha Thandizo kwa Yehova
1 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova.
2 Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi.
3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’
4 Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”
5 Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya,
6 Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine.
7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
8 Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9 Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa:
10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’
11 Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka?
12 Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi?
13 Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova.
15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova:
16 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
17 Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.
18 “Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo.
19 Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu.
20 Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”
Yehova Ayankha Pemphero la Hezekiya
21 Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.
22 Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa:
“Mwana wamkazi wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu,
akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
23 Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani?
Kodi iwe wafuwulira
ndi kumuyangʼana monyada ndani?
Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!
24 Kudzera mwa amithenga ako
iwe wanyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta anga ochuluka
ndafika pamwamba pa mapiri,
pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni.
Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri,
ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini.
Ndafika pa msonga pake penipeni,
nkhalango yake yowirira kwambiri.
25 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndi kumva madzi akumeneko
ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’
26 “Kodi sunamvepo
kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale?
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndazichitadi,
kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
27 Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu,
ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi.
Anali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu omera pa denga,
umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.
28 “Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe;
ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa,
ndiponso momwe umandikwiyira Ine.
29 Chifukwa umandikwiyira Ine
ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa
njira yomwe unadzera pobwera.
30 “Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi:
“Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha,
ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha,
koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola,
mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.
31 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire
adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.
32 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka.
Changu cha Yehova Wamphamvuzonse
chidzachita zimenezi.
33 “Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya:
“Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi uliwonse.
Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango
kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
34 Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,”
akutero Yehova.
35 “Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”
36 Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse!
37 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.
38 Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.