50
Tchimo la Israeli, Kumvera kwa Mtumiki
Yehova akuti,
“Kalata imene ndinasudzulira amayi
anu ili kuti?
Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole,
ndinakugulitsani kwa ati?
Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu;
amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu?
Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha?
Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani?
Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani?
Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu,
mitsinje ndinayisandutsa chipululu;
nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi;
ndipo zinafa ndi ludzu.
Ndinaphimba thambo ndi mdima
ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”
 
Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula
kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka.
Mmawa mulimonse amandidzutsa,
amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga,
ndipo sindinakhale munthu wowukira
ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya
masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu;
sindinawabisire nkhope yanga
anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
Popeza Ambuye Yehova amandithandiza,
sindidzachita manyazi.
Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi,
chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi,
ndaninso amene adzandiyimba mlandu?
Abwere kuti tionane maso ndi maso!
Mdani wanga ndi ndani?
Abweretu kuti tilimbane!
Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza.
Ndaninso amene adzanditsutsa?
Onse adzatha ngati chovala
chodyedwa ndi njenjete.
 
10 Ndani mwa inu amaopa Yehova
ndi kumvera mawu a mtumiki wake?
Aliyense woyenda mu mdima,
popanda chomuwunikira,
iye akhulupirire dzina la Yehova
ndi kudalira Mulungu wake.
11 Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto
ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu,
lowani mʼmoto wanu womwewo.
Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa.
Ndipo ine Yehova
ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.