63
Yehova Agonjetsa Anthu a Mitundu Ina
1 Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu,
atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira?
Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola,
akuyenda mwa mphamvu zake?
“Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo
ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”
2 Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,
ngati za munthu wofinya mphesa?
3 “Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa,
palibe ndi mmodzi yemwe anali nane.
Ndinawapondereza ndili wokwiya
ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali;
magazi awo anadothera pa zovala zanga,
ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
4 Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga;
ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
5 Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza.
Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza;
choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga,
ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
6 Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya;
ndipo ndinawasakaza
ndipo ndinathira magazi awo pansi.”
Matamando ndi Pemphero
7 Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,
ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.
Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.
Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake
Yehova wachitira nyumba ya Israeli
zinthu zabwino zambiri.
8 Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga,
ana anga amene sadzandinyenga Ine.”
Choncho anawapulumutsa.
9 Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,
ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.
Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,
anawanyamula ndikuwatenga
kuyambira kale lomwe.
10 Komabe iwo anawukira
ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera.
Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo
ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
11 Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana,
masiku a Mose mtumiki wake;
ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja,
pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo?
Ali kuti Iye amene anayika
Mzimu Woyera pakati pawo?
12 Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa
ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose?
Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona,
kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
13 amene anawayendetsa pa nyanja yozama?
Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu,
iwo sanapunthwe;
14 Mzimu Woyera unawapumulitsa
ngati mmene ngʼombe zimapumulira.
Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu
kuti dzina lanu lilemekezeke.”
15 Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka,
wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife.
Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti?
Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.
16 Koma Inu ndinu Atate athu,
ngakhale Abrahamu satidziwa
kapena Israeli kutivomereza ife;
Inu Yehova, ndinu Atate athu,
kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
17 Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu?
Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso?
Bwererani chifukwa cha atumiki anu;
mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.
18 Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa,
adani athu anasakaza malo anu opatulika.
19 Ife tili ngati anthu amene
simunawalamulirepo
ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.