8
Asiriya, Chida cha Yehova
Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira. Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”
Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’ Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
Yehova anayankhulanso ndi Ine;
“Popeza anthu a dziko ili akana
madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu,
ndipo akukondwerera Rezini
ndi mwana wa Remaliya,
nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa
madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo;
mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo.
Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse
ndi mʼmagombe ake onse.
Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira,
adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi.
Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse,
iwe Imanueli!”
 
Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere!
Tamverani, inu mayiko onse akutali.
Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
10 Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu,
kambiranani zochita, koma zidzalephereka,
pakuti Mulungu ali nafe.
Yehova Achenjeza Mneneri
11 Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:
12 “Usamanene kuti ndi chiwembu,
chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu
usamaope zimene anthuwa amaziopa,
ndipo usamachite nazo mantha.
13 Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,
ndiye amene uyenera kumuopa,
ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
14 ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika;
koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala
mwala wopunthwitsa,
mwala umene umapunthwitsa anthu,
thanthwe limene limagwetsa anthu.
Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
15 Anthu ambiri adzapunthwapo
adzagwa ndi kuthyokathyoka,
adzakodwa ndi kugwidwa.”
 
16 Manga umboniwu
ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
17 Ndidzayembekezera Yehova,
amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo.
Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.
18 Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.
19 Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo, 20 kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala. 21 Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo. 22 Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.