22
Mawu a Elifazi
Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
“Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu?
Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama?
Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
 
“Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula,
kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu?
Kodi machimo ako si opanda malire?
Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa;
umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
Sunawapatse madzi anthu otopa,
ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake,
munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu,
ndipo unapondereza ana amasiye.
10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira,
nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
11 nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu,
nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
 
12 “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?
Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
13 Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani?
Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
14 Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona
pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
15 Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale
imene anthu oyipa ankayendamo?
16 Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane,
maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
17 Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni!
Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
18 Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,
choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
 
19 “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera;
anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
20 Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka
ndipo moto wawononga chuma chawo!’
 
21 “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere;
ukatero udzaona zabwino.
22 Landira malangizo a pakamwa pake
ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.
23 Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa;
ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,
24 ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi,
golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.
25 Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako,
siliva wako wamtengowapatali.
26 Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse
ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
27 Udzamupempha ndipo adzakumvera,
ndipo udzapereka zimene unalonjeza.
28 Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi,
kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.
29 Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’
Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.
30 Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa,
ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”