32
Mawu a Elihu
1 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.
2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.
3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.
4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.
5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.
6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:
“Ine ndine wamngʼono,
inuyo ndinu akuluakulu,
nʼchifukwa chake ndimaopa,
ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;
anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,
mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
9 Si okalamba amene ali ndi nzeru,
si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.
10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;
inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
11 Ndadikira nthawi yonseyi,
ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
12 ineyo ndinakumvetseranidi.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;
palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;
Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,
ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.
15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;
mawu awathera.
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,
pakuti angoyima phee wopanda yankho?
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano;
nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri,
ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,
ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;
ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense,
kapena kuyankhula zoshashalika,
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,
Mlengi wanga akanandilanga msanga.”