4
1 “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,
bwererani kwa Ine,”
akutero Yehova.
“Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga
ndipo musasocherenso.
2 Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo
kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’
Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse
ndipo adzanditamanda.”
3 Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:
“Limani masala anu
musadzale pakati pa minga.
4 Dziperekeni nokha kwa Ine
kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,
inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.
Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,
chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo
popanda wina wowuzimitsa.
Adani Ochokera Kumpoto kwa Yuda
5 “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,
‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’
Ndipo fuwulani kuti,
‘Sonkhanani!
Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
6 Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!
Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!
Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,
kudzakhala chiwonongeko choopsa.”
7 Monga mkango umatulukira mʼngaka yake
momwemonso wowononga mayiko
wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.
Watero kuti awononge dziko lanu.
Mizinda yanu idzakhala mabwinja
popanda wokhalamo.
8 Choncho valani ziguduli,
lirani ndi kubuwula,
pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova
sunatichokere.
9 “Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,
ansembe adzachita mantha kwambiri,
ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”
akutero Yehova.
10 Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa;
12 koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”
13 Taonani, adani akubwera ngati mitambo,
magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu,
akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga.
Tsoka ilo! Tawonongeka!
14 Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.
Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
15 Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;
akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
16 Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,
lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,
‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,
akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
17 Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda,
chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ”
akutero Yehova.
18 “Makhalidwe anu ndi zochita zanu
zakubweretserani zimenezi.
Chimenechi ndiye chilango chanu.
Nʼchowawa kwambiri!
Nʼcholasa mpaka mu mtima!”
19 Mayo, mayo,
ndikumva kupweteka!
Aa, mtima wanga ukupweteka,
ukugunda kuti thi, thi, thi.
Sindingathe kukhala chete.
Pakuti ndamva kulira kwa lipenga;
ndamva mfuwu wankhondo.
20 Tsoka limatsata tsoka linzake;
dziko lonse lasanduka bwinja.
Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa,
mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.
21 Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,
ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?
22 Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;
iwo sandidziwa.
Iwo ndi ana opanda nzeru;
samvetsa chilichonse.
Ali ndi luso lochita zoyipa,
koma sadziwa kuchita zabwino.”
23 Ndinayangʼana dziko lapansi,
ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;
ndinayangʼana thambo,
koma linalibe kuwala kulikonse.
24 Ndinayangʼana mapiri,
ndipo ankagwedezeka;
magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25 Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;
mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;
mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja
pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.
27 Yehova akuti,
“Dziko lonse lidzasanduka chipululu
komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28 Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira
ndipo thambo lidzachita mdima,
pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,
ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”
29 Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,
anthu a mʼmizinda adzathawa.
Ena adzabisala ku nkhalango;
ena adzakwera mʼmatanthwe
mizinda yonse nʼkuyisiya;
popanda munthu wokhalamo.
30 Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja!
Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira
ndi kuvalanso zokometsera zagolide?
Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera,
ukungodzivuta chabe.
Zibwenzi zako zikukunyoza;
zikufuna kuchotsa moyo wako.
31 Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,
kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.
Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.
Atambalitsa manja awo nʼkumati,
“Kalanga ife! Tikukomoka.
Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”