12
Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa
Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
 
Sihoni mfumu ya Aamori,
amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
 
Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,
amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
 
Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
 
Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:
 
mfumu ya Yeriko imodzi
mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi
10 mfumu ya Yerusalemu imodzi
mfumu ya Hebroni imodzi
11 mfumu ya Yarimuti imodzi
mfumu ya Lakisi imodzi
12 mfumu ya Egiloni imodzi
mfumu ya Gezeri imodzi
13 mfumu ya Debri imodzi
mfumu ya Gederi imodzi
14 mfumu ya Horima imodzi
mfumu ya Aradi imodzi
15 mfumu ya Libina imodzi
mfumu ya Adulamu imodzi
16 mfumu ya Makeda imodzi
mfumu ya Beteli imodzi
17 mfumu ya Tapuwa imodzi
mfumu ya Heferi imodzi
18 mfumu ya Afeki imodzi
mfumu ya Lasaroni imodzi
19 mfumu ya Madoni imodzi
mfumu ya Hazori imodzi
20 mfumu ya Simuroni Meroni imodzi
mfumu ya Akisafu imodzi
21 mfumu ya Taanaki imodzi
mfumu ya Megido imodzi
22 mfumu ya Kadesi imodzi
mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi
23 mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi
mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi
24 mfumu ya Tiriza imodzi
mafumu onse pamodzi analipo 31.