19
Dziko la Simeoni
1 Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.
2 Dzikolo linaphatikiza zigawo izi:
Beeriseba (ndi Seba), Molada,
3 Hazari-Suwali, Bala, Ezemu,
4 Elitoladi, Betuli, Horima,
5 Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susa,
6 Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo.
7 Panalinso mizinda inayi iyi: Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani pamodzi ndi midzi yawo.
8 Dzikolo linaphatikizanso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baalati-Beeri, ndiye kuti Rama wa kummwera.
Ili ndi dziko limene mabanja a fuko la Simeoni analandira kukhala lawo.
9 Cholowa cha fuko la Simeoni chinatengedwa kuchokera ku gawo la Yuda chifukwa fuko la Yuda linali lalikulu kwambiri. Izi zinachititsa fuko la Simeoni kukhala mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.
Dziko la Zebuloni
10 Maere achitatu anagwera mabanja a fuko la Zebuloni:
Malire a dziko lawo anafika mpaka ku Saridi.
11 Malirewo anakwera kupita cha kumadzulo ku Marala nakafika ku Dabeseti ndi ku mtsinje wa kummawa kwa Yokineamu.
12 Kuchokera ku mbali ina ya Saridi malire anakhota kupita kummawa ku malire a Kisiloti-Tabori mpaka ku Daberati nakwera mpaka ku Yafiya.
13 Kuchokera kumeneko anabzola kulowa cha kummawa mpaka ku Gati-Heferi ndi ku Eti Kazini ndi kumaloza ku Neya njira ya ku Rimoni.
14 Mbali ya kumpoto malirewo analoza ku Hanatoni ndipo anakathera ku chigwa cha Ifita Eli.
15 Anaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Mizinda yonse inakwana khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yake.
16 Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndi imene mabanja a fuko la Zebuloni analandira.
Dziko la Isakara
17 Maere achinayi anagwera mabanja a fuko la Isakara.
18 Dziko lawo linaphatikiza zigawo izi:
Yezireeli, Kesuloti, Sunemu,
19 Hafaraimu, Sioni, Anaharati,
20 Rabiti, Kisoni, Ebezi,
21 Remeti, Eni Ganimu, Eni Hada ndi Beti-Pazezi.
22 Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake.
23 Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Isakara.
Dziko la Aseri
24 Maere achisanu anagwera mabanja a fuko la Aseri.
25 Gawo lawo linaphatikiza
Helikati, Hali, Beteni, Akisafu,
26 Alameleki, Amadi ndi Misali. Kumadzulo malire anafika ku Karimeli ndi Sihori Libinati.
27 Kenaka anakhotera kummawa kulowera ku Beti-Dagoni nafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifita Eli, ndipo anapita kumpoto ku Beti-Emeki ndi Neieli. Anapitirirabe kumpoto mpaka kukafika ku Kabuli,
28 Ebroni, Rehobu, Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni Wamkulu.
29 Kenaka malirewo anakhotera ku Rama ndi kupita ku mzinda wotetezedwa wa ku Turo. Kuchokera pamenepo malirewo anakhota kupita ku Hosa nakatulukira ku Nyanja, mʼchigawo cha Akizibu,
30 Uma, Afeki ndi Rehobu. Mizinda yonse inalipo 22 pamodzi ndi midzi yake.
31 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Aseri.
Dziko la Nafutali
32 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera mabanja a fuko la Nafutali.
33 Malire awo anayambira ku Helefu mpaka ku mtengo wa thundu wa ku Zaananimu, ndipo anapitirira nʼkukafika ku Adami Nekebu, Yabineeli mpaka ku Lakumi ndi kukathera ku Yorodani.
34 Tsono malirewo anakhotera kumadzulo kupita ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko anapita ku Hukoki, modutsa Zebuloni cha kummwera, Aseri cha kumadzulo ndi mtsinje wa Yorodani cha kummawa.
35 Mizinda yotetezedwa inali Zidimi, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti,
36 Adama, Rama, Hazori,
37 Kedesi, Ederi, Eni Hazori,
38 Yironi, Migidali Eli, Horemu, Beti-Anati ndi Beti-Semesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda 19 ndi midzi yake.
39 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yawo ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Nafutali.
Dziko la Dani
40 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera mabanja a fuko la Dani.
41 Gawo lawo linaphatikiza mizinda iyi:
Zora, Esitaoli, Iri Semesi,
42 Saalabini, Ayaloni, Itira,
43 Eloni, Timna, Ekroni,
44 Eliteke, Gibetoni, Baalati,
45 Yehudi, Beni Beraki, Gati-Rimoni,
46 Me-Yarikoni ndi Rakoni, pamodzi ndi dera loyangʼanana ndi Yopa.
47 Anthu a fuko la Dani atalandidwa dziko lawo, anapita kukathira nkhondo Lesemu. Iwo anapha anthu ake onse, nawulandiratu mzindawo, kuwusandutsa wawo ndi kumakhalamo. Tsono anatcha mzindawo dzina loti Dani popeza ndilo linali dzina la kholo lawo.
48 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Dani.
Dziko la Yoswa
49 Atatha kugawana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, Aisraeli anamupatsa Yoswa mwana wa Nuni chigawo chake.
50 Potsata zimene Yehova anawalamula, anamupatsa mzinda wa Timnati-Sera umene anawupempha. Mzindawu unali mʼdziko lamapiri la Efereimu. Iye anawumanga mzindawu ndi kukhazikikako.
51 Wansembe Eliezara, Yoswa ndi atsogoleri a mabanja onse a Israeli anagawa dziko lija zigawozigawo pogwiritsa ntchito maere pamaso pa Yehova. Izi zinachitika ku Silo pa khomo la tenti ya msonkhano. Choncho anamaliza kugawa dzikolo.