23
Kutsanzika kwa Yoswa
1 Panapita nthawi yayitali kuchokera pamene Yehova anakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraeli ndi adani awo owazungulira. Nthawi imeneyi nʼkuti Yoswa atakalamba, ali ndi zaka zambiri.
2 Yoswayo anayitanitsa Aisraeli onse pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi oyangʼanira anthu antchito ndipo anawawuza kuti, “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri.
3 Inu mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita kwa mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Ndi Yehova Mulungu wanu amene anakumenyerani nkhondo.
4 Tsono onani! Mitundu ya anthu otsalawa ndayipereka kwa mafuko anu pamodzi ndi mitundu ya anthu ya pakati pa Yorodani ndi Nyanja Yayikulu ya kumadzulo imene ndinayigonjetsa.
5 Yehova Mulungu wanu ndiye adzawathamangitsa pamaso panu. Mudzatenga dziko lawo monga Yehova anakulonjezerani.
6 “Choncho khalani amphamvu, ndipo samalani kuti mumvere zonse zimene zalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose. Musapatuke pa malamulo onse amene alembedwamo.
7 Musagwirizane ndi mitundu ya anthu imene yatsala pakati panu. Musatchule mayina a milungu yawo kapena kuyitchula polumbira. Musayitumikire kapena kuyigwadira.
8 Koma mukuyenera kugwiritsa Yehova Mulungu wanu, monga mwachitira mpaka lero lino.
9 “Yehova wapirikitsa patsogolo panu mitundu ya anthu ikuluikulu ndi yolimba. Mpaka lero palibe amene watha kulimbana nanu.
10 Aliyense wa inu atha kuthamangitsa anthu 1,000 chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye amakumenyerani nkhondo, monga momwe analonjezera.
11 Choncho samalitsani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.
12 “Koma ngati mubwerera mʼmbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalayi imene ili pakati panu ndi kumakwatirana nayo,
13 pamenepo mudziwe kuti Yehova, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu, koma idzakhala ngati msampha kwa inu kapenanso khwekhwe lokukolani. Idzakhala ngati zikwapu pa msana panu kapenanso ngati minga mʼmaso mwanu mpaka mutatha psiti mʼdziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.
14 “Aliyense wa inu akudziwa mu mtima mwake komanso mʼmoyo mwake kuti zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silinakwaniritsidwe.
15 Monga momwe Yehova Mulungu wanu wakuchitirani zabwino zonse zimene ananena kuti adzachita, Yehovayo angathenso kukuchitirani zoyipa zonse zimene waopseza, mpaka kukuchotsani mʼdziko lokoma limene anakupatsani.
16 Ngati muphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu, limene anakulamulirani nʼkumapita kukatumikira milungu ina ndi kuyigwadira, Yehova adzakukwiyirani, ndiye mudzachotsedwa mʼdziko labwinoli limene Yehova wakupatsani.”