15
Abiya Mfumu ya Yuda
1 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Nebati, Abiya anakhala mfumu ya Yuda,
2 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zitatu. Amayi ake anali Maaka, mwana wa Abisalomu.
3 Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide.
4 Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu;
5 pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti.
6 Panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu masiku onse a moyo wa Abiya.
7 Tsono ntchito zina za Abiya, ndi zina zonse anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu.
8 Ndipo Abiya anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Asa, mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Asa Mfumu ya Yuda
9 Mʼchaka cha makumi awiri cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda,
10 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu.
11 Asa anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake.
12 Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga.
13 Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni.
14 Ngakhale sanachotse malo opembedzerapo mafano, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova masiku onse a moyo wake.
15 Asa anabweretsa ku Nyumba ya Yehova zinthu zimene abambo ake anazipereka, ndiponso zinthu zimene iye mwini anazipereka: zagolide, siliva ndi ziwiya zotengera.
16 Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli nthawi yonse ya ulamuliro wawo.
17 Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda.
18 Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti,
19 “Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.”
20 Choncho Beni-Hadadi anamvera zimene ananena mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira magulu ake ankhondo ku mizinda ya Israeli. Ndipo iye anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Beti-Maaka ndi dera lonse la Kinereti kuphatikiza dziko lonse la Nafutali.
21 Baasa atamva zimenezi, anasiya kumangira linga Rama ndipo anakakhala ku Tiriza.
22 Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa.
23 Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi.
24 Ndipo Asa anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Nadabu Mfumu ya Israeli
25 Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri.
26 Nadabu anachita zoyipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira za abambo ake ndi mu uchimo womwe anachimwitsa nawo Israeli.
27 Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira.
28 Baasa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa, mfumu ya ku Yuda ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
29 Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo
30 chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli.
31 Tsono ntchito za Nadabu ndi zina zonse zimene anazichita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
32 Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli pa nthawi yonse ya ulamuliro wawo.
Baasa Mfumu ya Israeli
33 Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24.
34 Anachita zoyipa pamaso pa Yehova, nayenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchita tchimo lake limene linachimwitsa anthu a ku Israeli.