23
1 Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato.
2 Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
3 Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?”
Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
4 Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”
5 Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”
6 Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya.
7 Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.
8 Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa.
9 Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe.
10 Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri.
11 Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato.
12 Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.
13 Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu,
14 ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu.
15 Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe.
16 Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.”
17 (Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).
18 Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!”
19 (Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).
20 Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo.
21 Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22 Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
23 Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira.
24 Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo.
25 Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.
Kupachikidwa kwa Yesu
26 Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu.
27 Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira.
28 Yesu anatembenuka nati kwa iwo, “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu.
29 Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’
30 Kenaka,
“adzawuza mapiri kuti tigwereni ife;
zitunda kuti tiphimbeni ife.
31 Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”
32 Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa.
33 Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere.
34 Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35 Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
36 Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa,
37 ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38 Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39 Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”
40 Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi?
41 Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”
42 Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”
43 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”
Imfa ya Yesu
44 Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi,
45 pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati.
46 Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.
47 Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.”
48 Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka.
49 Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
50 Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama.
51 Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu.
52 Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu.
53 Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo.
54 Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.
55 Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira.
56 Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.