4
Kuyesedwa kwa Yesu
1 Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu,
2 kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.
3 Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.”
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”
5 Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi.
6 Ndipo anati kwa Iye, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wawo; pakuti anandipatsa ine, ndipo ndingathe kupereka kwa aliyense amene ndikufuna.
7 Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.”
8 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
9 Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano.
10 Pakuti kwalembedwa,
“Adzalamulira angelo ake za iwe
kuti akutchinjirize mosamala;
11 ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”
12 Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”
13 Mdierekezi atamaliza mayesero awa onse, anamusiya Iye kufikira atapeza mpata wina.
Yesu Akanidwa ku Nazareti
14 Yesu anabwerera ku Galileya mu mphamvu ya Mzimu Woyera, ndipo mbiri yake inafalikira ku madera onse a ku midzi.
15 Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo, ndipo aliyense ankamulemekeza.
16 Iye anapita ku Nazareti, kumene anakulira, ndipo pa tsiku la Sabata anakalowa mʼsunagoge, monga mwa chikhalidwe chake. Ndipo anayimirira kuti awerenge malemba.
17 Anamupatsa buku la mneneri Yesaya. Atalitsekula, anapeza pamalo pamene panalembedwa kuti,
18 “Mzimu wa Ambuye ali pa Ine;
chifukwa wandidzoza
kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka.
Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe
ndi kwa osaona kuti apenyenso,
kumasulidwa kwa osautsidwa,
19 ndi kulalikira za nthawi imene Ambuye adzakomere mtima anthu awo.”
20 Kenaka Iye anatseka bukulo, nalibwezera kwa wotumikira ndipo anakakhala pansi. Maso a aliyense mʼsunagogemo anali pa Iye,
21 ndipo anawawuza kuti, “Lero malemba awa akwaniritsidwa mmene mwamveramu.”
22 Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?”
23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, mudzandiwuza mwambi uwu: Singʼanga, dzichiritse wekha! Chitanso mʼmudzi wa kwanu kuno zimene ife tamva kuti Iwe unazichita ku Kaperenawo.”
24 Iye anapitiriza kuti, “Zoonadi, ndikukuwuzani kuti palibe mneneri amene amavomerezedwa ku mudzi kwawo.
25 Ine ndikukutsimikizirani kunali amayi ambiri amasiye mu Israeli mʼnthawi ya Eliya, kumwamba kutatsekedwa kwa zaka zitatu ndi theka ndipo kunali njala yayikulu mʼdziko lonselo.
26 Komabe Eliya sanatumidwe kwa mmodzi mwa iwo, koma kwa mkazi wamasiye wa ku Zerefati ku chigawo cha Sidoni.
27 Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”
28 Anthu onse mʼsunagogemo anapsa mtima atamva izi.
29 Anayimirira namutulutsira kunja kwa mzindawo, ndipo anamutengera pamwamba pa phiri pamene mzindawo unamangidwapo, ndi cholinga chakuti amuponyere ku phompho.
30 Koma Iye anangoyenda pakati pa gulu la anthulo nachokapo.
Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa
31 Kenaka Iye anapita ku Kaperenawo, mudzi wa ku Galileya, ndipo pa Sabata anayamba kuphunzitsa anthu.
32 Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro.
33 Mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu woyipa. Iye analira ndi mawu akulu, akuti
34 “Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
35 Yesu anachidzudzula kwambiri nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye.” Chiwandacho chinamugwetsa munthuyo pansi pamaso pa onse ndipo chinatuluka wosamupweteka.
36 Anthu onse anadabwa ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi chiphunzitso ichi ndi chotani? Ndi ulamuliro ndi mphamvu Iye akulamulira mizimu yoyipa ndipo ikutuluka!”
37 Ndipo mbiri yake inafalikira madera onse ozungulira.
Yesu Achiritsa Anthu Ambiri
38 Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize.
39 Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira.
40 Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa.
41 Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.
42 Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere.
43 Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.”
44 Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.