17
Za Kusadya Magazi
1 Yehova anawuza Mose kuti,
2 “Uza Aaroni ndi ana ake, pamodzi ndi Aisraeli onse kuti, ‘Chimene Yehova walamula ndi ichi:
3 Mwisraeli aliyense amene apha ngʼombe, mwana wankhosa kapena mbuzi mu msasa kapena kunja kwa msasa,
4 mʼmalo mobwera nayo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova ndi kuyipereka kuti ikhale nsembe ya Yehova, ameneyo wapalamula mlandu wa magazi, wakhetsa magazi ndipo ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.
5 Izi zili choncho kuti Aisraeli azibwera ndi nyama zawo za nsembe zimene akanaphera ku malo kwina kulikonse. Aisraeli azibwera nazo nyamazo kwa Yehova, kwa wansembe wokhala pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo aziphere pomwepo kuti zikhale nsembe za chiyanjano.
6 Wansembe awaze magazi ake pa guwa la Yehova limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo atenthe mafuta ake kuti atulutse fungo lokomera Yehova.
7 Motero asadzapherenso nsembe fano la mbuzi limene amachita nalo zadama. Limeneli ndi lamulo la muyaya kwa iwo ndi mibado ya mʼtsogolo.’ ”
8 “Uwawuze kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo amene amakhala pakati pawo akapereka nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse
9 popanda kubwera nayo pa khomo la tenti ya msonkhano kudzayipereka pamaso pa Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’ ”
10 “Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala pakati panu amene adya magazi, ndidzamufulatira ndipo ndidzamuchotsa pakati pa anthu anzake.
11 Pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi, ndipo ndawupereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amachotsa machimo chifukwa moyo uli mʼmenemo.
12 Choncho ndikuwawuza Aisraeli kuti, ‘Pasapezeke aliyense wa inu wodya magazi, ngakhale mlendo wokhala pakati panu.’ ”
13 “Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala pakati panu amene amasaka ndi kupha nyama zakuthengo kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuwakwirira ndi dothi,
14 chifukwa moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi ake. Nʼchifukwa chake ndinawawuza Aisraeli kuti, ‘Musamadye magazi a cholengedwa chilichonse, chifukwa moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.
15 “ ‘Munthu aliyense, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, amene amadya chilichonse chofa chokha, kapena chojiwa ndi zirombo, achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Kenaka adzakhala woyeretsedwa.
16 Koma ngati sachapa zovala zake ndi kusamba, adzasenzabe machimo ake.’ ”