18
Wamkulu mu Ufumu Wakumwamba
1 Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, “Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?”
2 Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo.
3 Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.
4 Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.
5 Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.
Za Kuchimwitsa Ena
6 “Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja.
7 Tsoka dziko lapansi chifukwa cha zinthu zimene ziyenera kubwera, koma tsoka kwa munthu amene abweretsa zotere!
8 Ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kulowa mʼmoyo wosatha wolumala kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kukaponyedwa ku moto wosatha.
9 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.”
Fanizo la Nkhosa Yotayika
10 “Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.”
11 (Mwana wa Munthu anabwera kudzapulumutsa chimene chinatayika).
12 “Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo?
13 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere.
14 Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike.
Za Mʼbale Amene Akuchimwirani
15 “Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo.
16 Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, ‘kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.’
17 Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.
18 “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.
19 “Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani.
20 Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”
Fanizo la Wantchito Wopanda Chifundo
21 Kenaka Petro anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Ambuye, kodi mʼbale wanga akandichimwira ndimukhululukire kokwanira kangati? Mpaka kasanu nʼkawiri?”
22 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza iwe kuti osati kasanu nʼkawiri, koma ka 70 kuchulukitsa ndi kasanu nʼkawiri.
23 “Nʼchifukwa chake, ufumu wakumwamba ukufanana ndi mfumu imene inafuna kuti antchito ake abweze ngongole.
24 Atangoyamba kulandira, anamubweretsa munthu kwa iye amene anakongola ndalama 10,000.
25 Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo.
26 “Wantchitoyo anagwada pamaso pake namupempha iye kuti, ‘Lezereni mtima ndipo ndidzabweza zonse.’
27 Bwana wakeyo anamuchitira chifundo, namukhululukira ngongoleyo ndipo anamulola apite.
28 “Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’
29 “Wantchito mnzakeyo anagwada namupempha iye kuti, ‘Lezere mtima ine, ndipo ndidzakubwezera.’
30 “Koma iye anakana. Mʼmalo mwake, anachoka nakamumangitsa kufikira atabweza ngongoleyo.
31 Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika.
32 “Pamenepo bwanayo anayitana wantchitoyo nati, ‘Iwe wantchito woyipa mtima, ndinakukhululukira ngongole yako yonse chifukwa unandipempha.
33 Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’
34 Ndi mkwiyo, bwana wakeyo anamupereka kwa oyangʼanira ndende kuti amuzuze mpaka atabweza zonse zimene anakongola.
35 “Umu ndi mmene Atate anga akumwamba adzachitira ndi aliyense wa inu ngati simukhululukira mʼbale wanu ndi mtima wonse.”