25
Fanizo la Anamwali Khumi
1 “Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati.
2 Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera.
3 Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta;
4 koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo.
5 Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.
6 “Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’
7 “Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo.
8 Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’
9 “Ochenjerawo anayankha, nati, ‘Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.’
10 “Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.
11 “Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’
12 “Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’
13 “Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi.”
Fanizo la Kagwiritsidwe Ntchito ka Ndalama
14 “Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake.
15 Wina anamupatsa ndalama 5,000, kwa wina 2,000 ndi kwa wina 1,000. Aliyense monga mwa nzeru zake. Pamenepo anapita pa ulendo wake.
16 Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja, anapita nthawi yomweyo nachita nazo malonda napindula 5,000 zina.
17 Chimodzimodzinso amene analandira 2,000 uja anapindula 2,000 zina.
18 Koma munthu amene analandira 1,000 uja, anapita nakumba dzenje nabisapo ndalama ya mbuye wake.
19 “Patapita nthawi yayitali, mbuye wa antchitowo anabwera nawayitana kuti afotokoze chimene anachita ndi ndalama zija.
20 Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, ‘Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.’
21 “Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
22 “Munthu amene anali ndi ndalama 2,000 uja anabweranso nati, ‘Ambuye munandisungitsa 2,000, onani, ndapindula 2,000 zinanso.’
23 “Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
24 “Kenaka munthu amene analandira ndalama 1,000 uja anabwera nati, ‘Ambuye ndinadziwa kuti ndinu munthu wowuma mtima, amene mumakolola pamene simunadzale ndi kututa kumene simunafese.
25 Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita ndi kukabisa ndalama yanuyo pa dzenje. Onani, si iyi ndalama yanu ija.’
26 “Mbuye wake anayankha nati, ‘Iwe wantchito woyipa ndi waulesi! Iwe umadziwa kuti ndimakolola pamene sindinadzale, ndi kututa kumene sindinafese.
27 Bwanji sunayike ndalama yanga kwa osunga ndalama kuti ine pobwera ndidzalandire ndalama yangayo pamodzi ndi chiwongoladzanja?
28 “ ‘Mulandeni ndalamayo, ndipo patsani iye amene ali ndi ndalama 10,000.
29 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, ndipo adzakhala nazo zochuluka. Aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.
30 Ndipo muponyeni wantchito wopanda phinduyu kunja, ku mdima kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’ ”
Nkhosa ndi Mbuzi
31 “Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba.
32 Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi.
33 Adzayika nkhosa ku dzanja lake lamanja ndi mbuzi ku lamanzere.
34 “Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko.
35 Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira,
36 ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’
37 “Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa?
38 Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani?
39 Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’
40 “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’
41 “Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake.
42 Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa,
43 ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’
44 “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’
45 “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’
46 “Amenewa adzapita ku chilango chosatha pamene olungama ku moyo wosatha.”