3
Kubwera kwa Ambuye
1 Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera.
2 Ndikufuna kuti mukumbukire mawu amene anayankhulidwa kale ndi aneneri oyera mtima ndiponso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu analipereka kudzera mwa atumwi.
3 Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa.
4 Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.”
5 Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi.
6 Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa.
7 Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.
8 Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi!
9 Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.
10 Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.
11 Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu
12 pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha.
13 Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.
14 Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye.
15 Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa.
16 Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.
17 Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa.
18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.