6
Fuko la Levi
1 Ana a Levi anali awa:
Geresoni, Kohati ndi Merari.
2 Ana a Kohati anali awa:
Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
3 Ana a Amramu anali awa:
Aaroni, Mose ndi Miriamu.
Ana a Aaroni anali awa:
Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara
4 Eliezara anabereka Finehasi,
Finehasi anabereka Abisuwa,
5 Abisuwa anabereka Buki,
Buki anabereka Uzi.
6 Uzi anabereka Zerahiya,
Zerahiya anabereka Merayoti,
7 Merayoti anabereka Amariya,
Amariya anabereka Ahitubi.
8 Ahitubi anabereka Zadoki,
Zadoki anabereka Ahimaazi.
9 Ahimaazi anabereka Azariya,
Azariya anabereka Yohanani,
10 Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),
11 Azariya anabereka Amariya,
Amariya anabereka Ahitubi,
12 Ahitubi anabereka Zadoki,
Zadoki anabereka Salumu,
13 Salumu anabereka Hilikiya,
Hilikiya anabereka Azariya,
14 Azariya anabereka Seraya,
ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.
15 Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.
16 Ana a Levi anali awa:
Geresomu, Kohati ndi Merari.
17 Mayina a ana a Geresomu ndi awa:
Libini ndi Simei.
18 Ana a Kohati anali awa:
Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
19 Ana a Merari anali awa:
Mahili ndi Musi.
Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:
20 Ana a Geresomu ndi awa:
Libini, Yehati,
Zima,
21 Yowa,
Ido, Zera
ndi Yeaterai.
22 Zidzukulu za Kohati ndi izi:
Aminadabu, Kora,
Asiri,
23 Elikana,
Ebiyasafu, Asiri,
24 Tahati, Urieli,
Uziya ndi Sauli.
25 Zidzukulu za Elikana ndi izi:
Amasai, Ahimoti,
26 Elikana, Zofai,
Nahati,
27 Eliabu,
Yerohamu, Elikana
ndi Samueli.
28 Ana a Samueli ndi awa:
Mwana wake woyamba anali Yoweli,
wachiwiri anali Abiya.
29 Zidzukulu za Merari ndi izi:
Mahili, Libini,
Simei, Uza,
30 Simea, Hagiya
ndi Asaya.
Oyimba mʼNyumba ya Mulungu
31 Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo.
32 Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.
33 Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa:
Ochokera ku banja la Kohati:
Hemani, katswiri woyimba,
anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,
34 mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu,
mwana wa Elieli, mwana wa Towa,
35 mwana wa Zufi, mwana wa Elikana,
mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
36 mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli,
mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
37 mwana wa Tahati, mwana wa Asiri,
mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,
38 mwana wa Izihari, mwana wa Kohati,
mwana wa Levi, mwana wa Israeli;
39 ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja:
Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,
40 mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya,
mwana wa Malikiya,
41 mwana wa Etini,
mwana wa Zera, mwana wa Adaya,
42 mwana wa Etani, mwana wa Zima,
mwana Simei,
43 mwana wa Yahati,
mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;
44 ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere:
Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi,
mwana wa Maluki,
45 mwana wa Hasabiya,
mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46 mwana wa Amizi, mwana wa Bani,
mwana wa Semeri,
47 mwana wa Mahili,
mwana wa Musi, mwana wa Merari,
mwana wa Levi.
48 Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu.
49 Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.
50 Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa:
Eliezara, Finehasi,
Abisuwa,
51 Buki,
Uzi, Zerahiya,
52 Merayoti, Amariya,
Ahitubi,
53 Zadoki
ndi Ahimaazi.
54 Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).
55 Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
56 Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.
57 Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa,
58 Hileni, Debri,
59 Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
60 Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.
61 Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.
62 Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.
63 Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
64 Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa.
65 Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.
66 Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.
67 Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri,
68 Yokineamu, Beti-Horoni,
69 Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.
70 Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.
71 Ageresomu analandira malo awa:
Kuchokera ku theka la fuko la Manase,
analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;
72 Kuchokera ku fuko la Isakara
analandira Kedesi, Daberati,
73 Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
74 kuchokera ku fuko la Aseri
analandira Masala, Abidoni,
75 Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
76 ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali
analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.
77 Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa:
kuchokera ku fuko la Zebuloni,
iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
78 Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko,
analandira Bezeri ku chipululu, Yaza,
79 Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
80 ndipo kuchokera ku fuko la Gadi
analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu,
81 Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.