16
Zaka Zotsiriza za Asa
1 Mʼchaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya Israeli inapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Anamangira mpanda mzinda wa Rama kuletsa aliyense kutuluka kapena kulowa mʼdziko la Asa mfumu ya Yuda.
2 Ndipo Asa anatenga siliva ndi golide ku malo osungirako a mʼNyumba ya Mulungu ndi ku nyumba yake yaufumu ndi kuzitumiza kwa Beni-Hadadi mfumu ya Aramu imene inkakhala mu Damasiko.
3 Iye anati, “Pakhale pangano pakati pa inu ndi ine, monga zinalili pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Taonani, ine ndikutumiza kwa inu siliva ndi golide. Tsopano thetsani mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti achoke kwa ine.”
4 Beni-Hadadi anagwirizana ndi mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira nkhondo ake kukathira nkhondo mizinda ya Israeli. Iwo anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Maimu ndi mizinda yonse yosungira chuma ya Nafutali.
5 Baasa atamva izi, anasiya kumanga Rama ndipo anayimitsa ntchito yakeyo.
6 Ndipo mfumu Asa anabwera ndi Ayuda onse, ndipo anachotsa miyala ndi matabwa ku Rama amene Baasa amagwiritsa ntchito. Ndi zimenezi Asa ankamangira Geba ndi Mizipa.
7 Nthawi imeneyi mlosi Hanani anabwera kwa Asa mfumu ya Yuda ndipo anati kwa iye, “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Aramu osati Yehova Mulungu wanu, gulu la ankhondo la mfumu ya ku Aramu lapulumuka mʼmanja mwanu.
8 Kodi Akusi ndi Alibiya sanali gulu lankhondo lamphamvu lokhala ndi magaleta ochuluka ndi okwera magaleta ake? Koma pamene inu munadalira Yehova, Iye anawapereka mʼdzanja lanu.
9 Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”
10 Asa anamupsera mtima mlosi uja chifukwa cha izi mwakuti anakwiya kwambiri namuyika mʼndende. Pa nthawi yomweyonso Asa anazunza mwankhanza anthu ena.
11 Ntchito zina za mfumu Asa, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli.
12 Mʼchaka cha 39 cha ufumu wake, Asa anayamba kudwala nthenda ya mapazi. Ngakhale nthendayo inali yaululu kwambiri, komabe iye sanafunefune Yehova, koma anafuna thandizo kwa asingʼanga.
13 Ndipo mʼchaka cha 41 cha ufumu wake, Asa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake.
14 Iye anayikidwa mʼmanda amene anadzisemera yekha mu Mzinda wa Davide. Anagoneka mtembo wake pa chithatha chimene anayikapo zonunkhira zamitundumitundu, ndipo anasonkha chimoto chachikulu pomuchitira ulemu.