35
Yosiya Achita Chikondwerero cha Paska
1 Yosiya anachita chikondwerero cha Paska wa Yehova mu Yerusalemu, ndipo mwana wankhosa wa Paska anaphedwa pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba.
2 Iye anasankha ansembe pa maudindo awo ndipo anawalimbikitsa pa ntchito ya mʼnyumba ya Yehova.
3 Iye anati kwa Alevi amene amalangiza Aisraeli onse omwe anadzipatula kwa Yehova: Ikani bokosi lopatulika mʼNyumba ya Mulungu amene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli anamanga. Lisamanyamulidwe pa mapewa anu. Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisraeli.
4 Mukhale mʼmagulu anu molingana ndi mabanja anu, molingana ndi momwe analembera Davide mfumu ya Israeli ndiponso mwana wake Solomoni.
5 “Muziyima ku malo opatulika pamodzi ndi gulu la Alevi oyimira gulu lililonse lalingʼono la mabanja a abale anu amene ndi anthu wamba.
6 Muzipha ana ankhosa a Paska, muzidzipatula nokha ndi kuwakonzera abale anu ana ankhosa awo, kuchita zimene Yehova analamulira mwa Mose.”
7 Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu.
8 Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300.
9 Konaniya nayenso pamodzi ndi Semaya ndi Netaneli, abale ake ndi Hasabiya, Yeiyeli ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, anapereka nsembe za Paska 5,000 ndi ngʼombe 500 kwa Alevi.
10 Mwambo unakonzedwa ndipo ansembe anayima pamalo pawo pamodzi ndi Alevi mʼmagulu awo monga mfumu inalamulira.
11 Ana ankhosa a Paska anaphedwa ndipo ansembe anawaza magazi amene anaperekedwa kwa iwo pamene Alevi anali kusenda nyamazo.
12 Iwo anayika padera nsembe zopsereza kuti azipereke kwa magulu angʼonoangʼono a mabanja a anthu kuti apereke kwa Yehova monga zinalembedwa mʼbuku la Mose. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi ngʼombe.
13 Anawotcha nyama za Paska monga momwe zinalembedwera ndi kuwiritsa zopereka zopatulika mʼmiphika, mʼmitsuko ndi mʼziwaya ndipo anazipereka mofulumira kwa anthu onse.
14 Izi zitatha, anakonza zawo ndi za ansembe chifukwa ansembe, zidzukulu za Aaroni, anali otanganidwa kupereka nsembe zopsereza ndi mafuta a nyama mpaka madzulo. Choncho Alevi amakonza zawo ndi za ansembe, ana a Aaroni.
15 Anthu oyimba nyimbo, zidzukulu za Asafu, anali pa malo awo potsata zomwe analemba Davide, Asafu, Hemani ndi Yedutuni mlosi wa mfumu. Alonda apazipata anali pa chipata chilichonse ndipo kunali kosafunika kuti achoke pa ntchito yawo, poti abale awo Alevi ankawakonzera zonse.
16 Kotero pa nthawi imeneyi ntchito yonse ya Yehova ya chikondwerero cha Paska ndi nsembe zopsereza pa guwa la Yehova inachitika monga analamulira mfumu Yosiya.
17 Aisraeli amene analipo anachita chikondwerero cha Paska pa nthawi imeneyi ndi kuchita mwambo wa chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti, kwa masiku asanu ndi awiri.
18 Paska yofanana ndi iyi sinachitikepo ku Israeli kuyambira nthawi ya Samueli ndipo palibe mmodzi mwa mafumu a Israeli anachitapo chikondwerero cha Paska ngati anachitira Yosiya pamodzi ndi ansembe, Alevi ndi Ayuda onse ndi Aisraeli amene anali pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu.
19 Chikondwerero cha Paska ichi chinachitika mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya.
Imfa ya Yosiya
20 Zimenezi zitachitika, pamene Yosiya anakonzanso Nyumba ya Mulungu, Neko mfumu ya Igupto inapita kukachita nkhondo ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye.
21 Koma Neko anatumiza amithenga kwa iye kunena kuti, “Kodi pali mkangano wanji pakati pa iwe ndi ine, iwe mfumu ya Yuda? Ine sindikuthira nkhondo iwe pa nthawi ino, koma nyumba imene ndili nayo pa nkhondo. Mulungu wandiwuza kuti ndifulumize choncho leka kutsutsana ndi Mulungu amene ali ndi ine, mwina adzakuwononga.”
22 Komabe Yosiya sanatembenuke kumusiya iyeyo, koma anadzizimbayitsa ndi kukalowa mʼnkhondo. Iye sanamvere zimene Neko ananena molamulidwa ndi Mulungu koma anapita kukamenyana naye ku chigwa ku Megido.
23 Anthu oponya mivi analasa mfumu Yosiya, ndipo iye anawuza akuluakulu ake, “Chotseni. Ndavulazidwa kwambiri.”
24 Choncho anamuchotsa iye mʼgaleta lake, ndipo anamuyika mʼgaleta lina limene anali nalo ndipo anabwera naye ku Yerusalemu kumene anamwalirira. Iye anayikidwa mʼmanda a makolo ake. Ndipo Ayuda ndi Yerusalemu yense anamulira.
25 Yeremiya anapeka nyimbo za maliro chifukwa cha Yosiya, ndipo mpaka lero lino amuna ndi akazi onse oyimba amakumbukira Yosiya pa nyimbo zawo za maliro. Izi zinakhala mwambo mu Israeli ndipo zinalembedwa mʼNyimbo za Maliro.
26 Zochitika zina za ulamuliro wa Yosiya ndi ntchito za kudzipereka kwake, monga zinalembedwa mʼMalamulo a Yehova,
27 zochitika zonse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.