5
1 Pamene ntchito yonse imene Solomoni anagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka; siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Mulungu.
Bokosi la Chipangano Libweretsedwa mʼNyumba ya Mulungu
2 Kenaka Solomoni anasonkhanitsa akuluakulu a Israeli mu Yerusalemu, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, mzinda wa Davide.
3 Ndipo Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa mfumu nthawi ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri.
4 Akuluakulu onse a Israeli atafika, Alevi ananyamula Bokosi la Chipangano,
5 ndipo anabwera nalo bokosi lija pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula,
6 ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.
7 Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a Akerubi.
8 Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira.
9 Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika, koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino.
10 Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
11 Kenaka ansembe anatulukamo mʼMalo Opatulika. Ansembe onse amene anali mʼmenemo anali atadziyeretsa posayangʼaniranso magulu awo ochokera.
12 Alevi onse amene anali oyimba: Asafu, Hemani, Yedutuni ndi ana ndiponso abale awo, amayima mbali ya kummawa kwa guwa lansembe atavala zovala zofewa zosalala akuyimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe. Ansembe onse amene amayimba malipenga analipo 120 pamodzi.
13 Oyimba malipenga ndi oyimba nyimbo aja amayimba mogwirizana, monga liwu la munthu mmodzi, kutamanda ndi kuyamika Yehova. Mogwirizana ndi malipenga, ziwaya zamalipenga ndi zida zina, anakweza mawu awo motamanda Yehova poyimba kuti,
“Yehova ndi wabwino;
chikondi chake chikhala mpaka muyaya.”
Ndipo Nyumba ya Mulungu wa Yehova inadzaza ndi mtambo,
14 choncho ansembe sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.