16
Davide ndi Ziba
1 Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo.
2 Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?”
Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.”
3 Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?”
Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”
4 Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.”
Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.”
Simei Atukwana Davide
5 Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera.
6 Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake.
7 Potukwana, Simeiyo amati, “Choka iwe, choka iwe, munthu wopha anthu, munthu wachabechabe iwe!
8 Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!”
9 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.”
10 Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ”
11 Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero.
12 Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.”
13 Kotero Davide ndi anthu ake anapitirira kuyenda mu msewu pamene Simei amayenda mʼmbali mwa phiri moyangʼanana naye akutukwana ndi kuponya miyala pamene amayenda nʼkumamutsiranso dothi.
14 Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula.
Malangizo a Husai ndi Ahitofele
15 Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye.
16 Tsono Husai Mwariki bwenzi la Davide anapita kwa Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu! Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”
17 Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?”
18 Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse.
19 Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.”
20 Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?”
21 Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.”
22 Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona.
23 Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.