7
Lonjezo la Mulungu kwa Davide
Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira, mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.”
Natani anayankha mfumu kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu chifukwa Yehova ali nanu.”
Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati,
“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo? Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti. Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense atsogoleri awo, amene ndinamulamula kuweta anthu anga Aisraeli kuti, nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”
“Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. 10 Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja, 11 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse.
“ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako: 12 Masiku ako akadzatha ndipo ukadzakapuma ndi makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, imene idzachokera mʼthupi mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 13 Iye ndiye amene adzamangire nyumba Dzina langa, ndipo Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. 14 Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu. 15 Koma sindidzasiya kumukonda, monga ndinachitira ndi Sauli, amene ndinamuchotsa iwe usanakhale mfumu. 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ”
17 Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.
Pemphero la Davide
18 Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati:
“Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?” 19 Ndipo kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Kodi umu ndi mmene mumachitira ndi munthu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse?
20 Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu? Pakuti Inu Ambuye Wamphamvuzonse mukumudziwa mtumiki wanu. 21 Chifukwa cha mawu anu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwachiwulula kwa mtumiki wanu.
22 Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu. 23 Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 24 Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.
25 “Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera, 26 kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
27 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 28 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 29 Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”