39
Nthumwi Zochokera ku Babuloni
1 Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira.
2 Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
3 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?”
Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
4 Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?”
Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
5 Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse:
6 Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe.
7 Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”
8 Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”